Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 1:3 - Buku Lopatulika

Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse mu Israele akutuluka ku nkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse m'Israele akutuluka ku nkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iwe ndi Aroni muŵerenge anthu, gulu ndi gulu, a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, ndiye kuti anthu onse a ku Israele amene angathe kumenya nkhondo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali.

Onani mutuwo



Numeri 1:3
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo mu Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu.


Ana a Rubeni, ndi a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ngwazi, amuna akugwira chikopa ndi lupanga, ndi kuponya mivi, ozolowera nkhondo, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zinai mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi akutuluka kunkhondo.


Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akutulukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi chikopa.


Ndipo muzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m'dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.


Yense wakupita kwa owerengedwawo, wa zaka makumi awiri ndi wa mphambu zake, apereke choperekacho kwa Yehova.


Munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kunka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.


mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwani konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;


Werenga khamu lonse la ana a Israele, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akutulukira kunkhondo mu Israele.


Werenga ana a Levi monga mwa nyumba ya makolo ao, monga mwa mabanja ao; uwawerenge mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu.


Anthu adakwerawo kutuluka mu Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse;


Maulendo a ana a Israele amene anatuluka m'dziko la Ejipito monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa.


kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako.


Munthu akatenga mkazi watsopano, asatuluke ku nkhondo, kapena asamchititse kanthu kalikonse; akhale waufulu kunyumba yake chaka chimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo.


Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.