Numeri 1:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse mu Israele akutuluka ku nkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse m'Israele akutuluka ku nkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Iwe ndi Aroni muŵerenge anthu, gulu ndi gulu, a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, ndiye kuti anthu onse a ku Israele amene angathe kumenya nkhondo. Onani mutuwo |
Amaziya anasonkhanitsa anthu a ku Yuda ndipo anawapatsa zochita molingana ndi mabanja awo kukhala anthu olamulira 1,000, ndi olamulira 100 pa Ayuda onse ndi Benjamini. Ndipo iye anawerenga amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo napeza kuti analipo amuna 300,000 okonzeka kugwira ntchito ya usilikali, okhoza kugwiritsa ntchito mkondo ndi chishango.