Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 1:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Werengani Aisraeli onse mʼmafuko awo ndi mʼmabanja awo, lemba dzina la munthu wamwamuna aliyense, mmodzimmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Werenga khamu lonse la ana a Israele, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzimmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Werenga khamu lonse la ana a Israele, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzimmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Uŵerenge anthu a mpingo wonse wa Aisraele potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Ulembe dzina la munthu wamwamuna aliyense mmodzimmodzi.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:2
16 Mawu Ofanana  

Aisraeli anayenda ulendo kuchokera ku Ramesesi mpaka kukafika ku Sukoti. Anthu aamuna oyenda pansi analipo 600,000 osawerengera akazi ndi ana.


“Pamene ukuchita kalembera wa Aisraeli, munthu aliyense ayenera kupereka kwa Yehova chowombolera moyo wake pamene akuwerengedwa. Motero mliri sudzabwera pa iwo pamene ukuwawerenga.


Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika.


Munthu aliyense amapereka beka imodzi, kufanana ngati makilogalamu 6, potsata muyeso wa ku malo wopatulika. Kuchokera kwa aliyense amene anawerengedwa kuyambira zaka 20 kapena kuposerapo, amuna onse analipo 603,550.


ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi


monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:


Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa