Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 1:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta adalankhula ndi Mose ku chipululu cha Sinai, m'chihema chamsonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiŵiri, chaka chachiŵiri atatuluka ku dziko la Ejipito, ndipo adamuuza kuti,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:1
15 Mawu Ofanana  

Patapita zaka 480 Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto, chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomoni mu Israeli, mwezi wa Zivi, umene ndi mwezi wachiwiri, Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova.


Ana a Israeli aja anafika ku chipululu cha Sinai pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere mʼdziko la Igupto.


Atachoka ku Refidimu, anafika ku Sinai, ndipo Aisraeli anamangako misasa yawo moyangʼanana ndi phirilo.


Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli.


Kotero anayimika chihema tsiku loyamba la mwezi woyamba mʼchaka chachiwiri.


“Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi.


26 Yehova anayitana Mose mu tenti ya msonkhano. Iye anati,


Amenewa ndi malamulo amene Yehova anamupatsa Mose pa Phiri la Sinai kuti awuze Aisraeli.


ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi


Nthawi yomweyo Yehova anati kwa Mose, Aaroni ndi Miriamu, “Bwerani ku tenti ya msonkhano nonse atatu.” Ndipo atatuwo anapitadi kumeneko.


Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai pa mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, nati,


Mʼchaka cha makumi anayi, pa tsiku loyamba la mwezi 11, Mose anafotokozera Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamula zokhudza iwowo.


Panapita zaka 38 kuchokera pa nthawi imene tinachoka ku Kadesi Barinea mpaka pamene tinawoloka Chigwa cha Zeredi. Pa nthawi imeneyi nʼkuti mʼbado wonse wa anthu ankhondowo utawonongeka ku msasa monga Yehova anawalumbirira.


Yehova Mulungu wanu wakudalitsani mʼntchito zonse za manja anu. Iye wakuyangʼanirani pa ulendo wanu wodutsa mʼchipululu chachikulu. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu mʼzaka makumi anayi, ndipo simunasowe kalikonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa