Nehemiya 8:3 - Buku Lopatulika
Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.
Onani mutuwo

Tsono Ezara adaŵerenga bukulo atayang'ana bwalo la Chipata cha Madzi, kuyambira m'mamaŵa mpaka pa masana, pamaso pa amuna ndi akazi omwe, ndiponso onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Ndipo anthu onsewo ankatchera makutu kuti amve zoŵerengazo.
Onani mutuwo
Choncho Ezara anawerenga bukulo atayangʼana bwalo la Chipata cha Madzi kuyambira mmawa mpaka masana pamaso pa amuna, akazi ndi onse amene ankamvetsa bwino zinthu. Ndipo anthu onse anatchera khutu kuti amve malamulowo.
Onani mutuwo