Machitidwe a Atumwi 13:27 - Buku Lopatulika27 Pakuti iwo akukhala mu Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikire Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Pakuti iwo akukhala m'Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikira Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 Anthu a ku Yerusalemu ndi atsogoleri awo sanazindikire Yesu, komabe pomuweruza Yesu anakwaniritsa mawu a Aneneri amene amawerengedwa Sabata lililonse. Onani mutuwo |