Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 8:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndipo anthu onse adasonkhana pamodzi pa bwalo la patsogolo pa Chipata cha Madzi. Tsono anthuwo adamuuza Ezara, amene anali mlembi, wansembe ndi mphunzitsi wa malamulo, kuti abwere ndi buku la Malamulo a Mose limene Chauta adaapatsa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi pabwalo limene lili patsogolo pa Chipata cha Madzi. Iwo anawuza mlembi Ezara kuti abwere ndi buku la malamulo a Mose limene Yehova anapereka kwa Aisraeli.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 8:1
25 Mawu Ofanana  

Nikwera mfumu kunka kunyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu pamodzi naye, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse aang'ono ndi aakulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.


Ndipo Hilikiya anayankha nati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Hilikiya napereka buku kwa Safani.


Nikwera mfumu kunyumba ya Yehova ndi amuna onse a mu Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu, ndi ansembe ndi Alevi, ndi anthu onse aakulu ndi aang'ono; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.


Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,


Pakuti Ezara adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa mu Israele malemba ndi maweruzo.


Malemba a kalatayo mfumu Arita-kisereksesi anampatsa Ezara wansembe mlembi, ndiye mlembi wa mau a malamulo a Yehova, ndi malemba ake kwa Israele, ndi awa:


Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.


Awa anakhala m'masiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndi m'masiku a Nehemiya kazembe, ndi a Ezara wansembe mlembiyo.


ndi ku Chipata cha ku Chitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mzinda wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku Chipata cha Madzi kum'mawa.


Koma antchito a m'kachisi okhala mu Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo.


Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la Chipata cha Efuremu.


Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.


Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


Pamenepo anatenga zimene Mose anawauza, napita nazo pakhomo pa chihema chokomanako; ndi msonkhano wonse unasendera kufupi nuimirira pamaso pa Yehova.


Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake, mlembi aliyense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m'chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose;


Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina;


pakufika Israele wonse kuoneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene adzasankha, muzilalikira chilamulo ichi pamaso pa Israele wonse, m'makutu mwao.


Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.


Ndipo anthu onse anauka ngati munthu mmodzi, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzamuka kuhema kwake, kapena kupatukira nyumba yake,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa