Nehemiya 7:73 - Buku Lopatulika73 Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oimbira, ndi anthu ena, ndi antchito a m'kachisi, ndi Aisraele onse. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri ana a Israele anakhala m'midzi mwao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201473 Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oimbira, ndi anthu ena, ndi Anetini, ndi Aisraele onse. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri ana a Israele anakhala m'midzi mwao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa73 Motero ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, anthu oimba nyimbo, ambiri mwa anthu wamba, atumiki a m'Nyumba ya Mulungu ndi Aisraele ena onse, ankakhala m'mizinda mwao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero73 Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo. Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo. Onani mutuwo |