Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 7:72 - Buku Lopatulika

72 Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri, ndi malaya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

72 Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya mina ya siliva zikwi ziwiri, ndi malaya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

72 Ndipo anthu onse otsala adapereka ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndalama zasiliva zamakilogaramu 140, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 67.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

72 Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 7:72
5 Mawu Ofanana  

Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulida mneneri wamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala za mfumu; analikukhala iye mu Yerusalemu m'dera lachiwiri, nalankhula naye.


Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri, ana a Israele ali m'midzimo, anthuwo anasonkhana ngati munthu mmodzi ku Yerusalemu.


Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, antchito a m'kachisi, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira,


Enanso a akulu a nyumba za makolo anapereka kuchuma cha ntchitoyi, madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri.


Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oimbira, ndi anthu ena, ndi antchito a m'kachisi, ndi Aisraele onse. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri ana a Israele anakhala m'midzi mwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa