ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko:
Nehemiya 7:7 - Buku Lopatulika ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisraele ndiwo: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisraele ndiwo: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adabwera pamodzi ndi atsogoleri aŵa: Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana. Nachi chiŵerengero cha anthu aamuna a Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana. Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere: |
ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko:
Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.
Awa tsono ndi akulu a dziko okhala mu Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi antchito a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni.
Ndipo ansembe ndi Alevi amene anakwera ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa, ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,
Ndi Yesuwa anabala Yoyakimu, ndi Yoyakimu anabala Eliyasibu ndi Eliyasibu anabala Yoyada,
Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja chisoni chifukwa ninji popeza sudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mtima. Pamenepo ndinachita mantha aakulu.
Ana a dziko amene anakwera kuchokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:
Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; chilichonse chinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.
Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,