Ezara 5:2 - Buku Lopatulika2 Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Atamva mauwo, Zerubabele mwana wa Sealatiele ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki adanyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Aneneri a Mulunguwo nawonso anali nawo pamodzi namaŵathandiza. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Pambuyo pake Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki ananyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Ndipo aneneri a Mulungu anali nawo pamodzi, kuwathandiza. Onani mutuwo |
Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova.