Hagai 1:1 - Buku Lopatulika1 Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chimodzi, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga. Uthengawu, wopita kwa Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, ndiponso kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, udati, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Chaka chachiwiri cha Mfumu Dariyo, tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chimodzi, Yehova anapatsa mneneri Hagai uthenga wopita kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, ndiponso kwa mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki: Onani mutuwo |
Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova.