Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mika 5:9 - Buku Lopatulika

Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Inu Aisraele, mudzapambana adani anu, ndipo adani anu onsewo adzaonongeka.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mudzagonjetsa adani anu, ndipo adani anu onse adzawonongeka.

Onani mutuwo



Mika 5:9
15 Mawu Ofanana  

Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; musaiwale ozunzika.


Potero anawasamulira dzanja lake, kuti awagwetse m'chipululu:


Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse, dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.


ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzachotsa seta wako wonse:


Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.


Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.


Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.


Ndipo mthenga wa Yehova anatuluka, naphaipha m'zithando za Asiriya, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.


ndipo ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magaleta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake.


Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa mu Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa mu Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake.