Zekariya 9:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa mu Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa mu Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa m'Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa m'Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efuremu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu. Uta wankhondo adzauthyola. Mfumu yanu idzachititsa mtendere pakati pa mitundu yonse ya anthu. Adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndiponso kuchokera ku Mtsinje wa Yufurate mpaka ku mathero a dziko lapansi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efereimu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu, ndipo uta wankhondo udzathyoka. Mfumuyo idzabweretsa mtendere pakati pa mitundu ya anthu. Ulamuliro wake udzayambira ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndipo kuchokera ku Mtsinje (Yufurate) mpaka ku malekezero a dziko lapansi. Onani mutuwo |