Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.
Mika 4:4 - Buku Lopatulika Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma munthu aliyense azidzangodzikhalira mwamtendere patsinde pa mtengo wake wamphesa, ndi patsinde pa mkuyu wake. Palibe amene adzaŵachititsa mantha, pakuti mwiniwake, Chauta Wamphamvuzonse, wanena zimenezi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthu aliyense adzakhala pansi pa tsinde pa mtengo wake wa mpesa ndi pa tsinde pa mtengo wake wamkuyu, ndipo palibe amene adzawachititse mantha, pakuti Yehova Wamphamvuzonse wayankhula. |
Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.
Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.
koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.
Tsiku limenelo, ati Yehova wa makamu, chikhomo chokhomeredwa polimba udzasukusika; nudzaguluka, ndi kugwa, ndi katundu wopachikidwapo adzadulidwa; pakuti Yehova wanena.
Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.
Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asiriya itere, Mupangane nane, tulukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zake, ndi nkhuyu zake, namwe yense madzi a pa chitsime chake;
ndipo ulemerero wa Yehova udzavumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena chomwecho.
M'chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe.
pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa cholowa cha kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo.
Ndipo ndidzaziikira abusa amene adzazidyetsa; sadzaopanso, kapena kutenga nkhawa, sipadzasowa mmodzi yense, ati Yehova.
Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israele; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutali, ndi mbeu zako kudziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala chete, palibe amene adzamuopsa.
Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.
Ndipo sadzakhalanso chakudya cha amitundu, ndi chilombo chakuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.
nudzati, Ndidzakwera kunka kudziko la midzi yopanda malinga, ndidzanka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mapiringidzo, kapena zitseko;
Ndipo adzasenza manyazi ao, ndi zolakwa zao zonse, zimene anandilakwira nazo, pokhala mosatekeseka iwo m'dziko lao, opanda wina wakuwaopsa;
Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.
Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.
Otsala a Israele sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.
Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.