Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 3:10 - Buku Lopatulika

10 Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsiku limenelo, nonsenu mudzaitanizana kuti mukakondwerere ufulu wanu, aliyense atakhala pa mtengo wake wa mphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Chauta Wamphamvuzonse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “ ‘Tsiku limenelo aliyense adzayitana mnzake kuti akhale pansi pa mtengo wamphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 3:10
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.


Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.


Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.


Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asiriya itere, Mupangane nane, tulukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zake, ndi nkhuyu zake, namwe yense madzi a pa chitsime chake;


Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Nyumba ndi minda ndi minda yampesa idzagulidwanso m'dziko muno.


Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.


Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa