Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mika 3:3 - Buku Lopatulika

inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mumandidyera anthu anga, mumachita ngati kumaŵasenda, kuphwanya mafupa ao, ndi kumaŵachekera mumphika ngati nyama.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

inu amene mumadya anthu anga, mumasenda khungu lawo ndi kuphwanya mafupa awo; inu amene mumawadula nthulinthuli ngati nyama yokaphika?”

Onani mutuwo



Mika 3:3
11 Mawu Ofanana  

Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova.


Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.


Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni; kuti adye osauka kuwachotsa kudziko, ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu.


Yehova adzalowa m'bwalo la milandu ndi okalamba a anthu ake, ndi akulu ake: Ndinu amene mwadya munda wampesa, zofunkha za waumphawi zili m'nyumba zanu;


muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? Ati Ambuye, Yehova wa makamu.


ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mzinda uwu ndi mphika, ife ndife nyama.


Longamo pamodzi ziwalo zake, ziwalo zonse zokoma, mwendo wathako ndi wamwamba; uudzaze ndi mafupa osankhika.


Tamverani ichi, inu akumeza aumphawi, ndi kuwatha ofatsa m'dziko, ndi kuti,


Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.


Akalonga ake m'kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.