Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye kutsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.
Mateyu 8:18 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke kutsidya lina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke kutsidya lina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu adaona chinamtindi cha anthu amene adaamuzinga, adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu ataona gulu la anthu litamuzungulira, analamula kuti awolokere kutsidya lina la nyanja. |
Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye kutsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.
Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.
Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.
Ndipo panali limodzi la masiku aja, Iye analowa m'ngalawa, ndi ophunzira ake; nati kwa iwo, Tiolokere kutsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo.
Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.