Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 8:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m'ngalawa, nachoka kunka ku tsidya lija.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m'ngalawa, nachoka kunka ku tsidya lija.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Atatero, Yesu adaŵasiya, naloŵanso m'chombo kuwolokera ku tsidya lina.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndipo anawasiya, nalowanso mʼbwato ndi kuwolokera tsidya lina.

Onani mutuwo Koperani




Marko 8:13
15 Mawu Ofanana  

Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao, ayende monga mwa uphungu waowao.


Ndipo pamene anthu awa, kapena mneneri, kapena wansembe, adzakufunsa iwe, kuti, Katundu wa Yehova ndi chiyani? Pamenepo uziti kwa iwo, Katundu wanji? Ndidzakuchotsani inu, ati Yehova.


Efuremu waphatikana ndi mafano, mlekeni.


Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera.


Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.


Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.


Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno!


Ndipo ophunzira adaiwala kutenga mikate, ndipo analibe mkate m'ngalawa koma umodzi wokha.


Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha aakulu. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, nabwerera.


Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako. Izi Yesu analankhula, nachoka nawabisalira.


Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.


Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.


Ndipo m'mene tidalowa m'ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa