Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 8:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Yesu adadzumira mu mtima nati, “Kodi bwanji anthu a mbadwo uno amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa? Ndithu ndikunenetsa kuti anthu a mbadwo unowu sadzachiwona chizindikiro akufunacho.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 8:12
15 Mawu Ofanana  

Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Pomwepo alembi ndi Afarisi ena anayankha Iye nati, Mphunzitsi, tifuna kuona chizindikiro cha Inu.


Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya, nachokapo.


Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.


Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.


nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Efata, ndiko, Tatseguka.


Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m'ngalawa, nachoka kunka ku tsidya lija.


Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.


Ndipo m'mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa