Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi.
Mateyu 4:11 - Buku Lopatulika Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Satana adamsiya, angelo nkubwera kumadzamutumikira Yesuyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye. |
Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi.
Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?
nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala.
Ndipo anakhala m'chipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zilombo, ndipo angelo anamtumikira.
Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.
Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.
Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?
Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu.