Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 28:3 - Buku Lopatulika

Kuonekera kwake kunali ngati mphezi, ndi chovala chake choyeretsa ngati matalala;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Kuonekera kwake kunali ngati mphezi, ndi chovala chake choyeretsa ngati matalala;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Maonekedwe ake anali ngati a mphezi, ndipo chovala chake chinali choyera chambee.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Maonekedwe ake anali ngati mphenzi ndipo zovala zake zinali mbuu ngati matalala.

Onani mutuwo



Mateyu 28:3
14 Mawu Ofanana  

Amene ayesa mphepo amithenga ake; lawi la moto atumiki ake;


Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka.


ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.


ndipo ndi kuopsa kwake alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa.


Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala kumbali ya kudzanja lamanja, wovala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa.


ndipo zovala zake zinakhala zonyezimira, zoyera mbuu; monga ngati muomba wotsuka nsalu padziko lapansi sangathe kuziyeretsai.


ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona.


Ndipo pakukhala iwo chipenyerere kumwamba pomuka Iye, taonani, amuna awiri ovala zoyera anaimirira pambali pao;


Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wovala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto;


Zitatha izi ndinaona mngelo wina wakutsika mu Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukulu; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wake.