Danieli 7:9 - Buku Lopatulika9 Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pa mutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 “Ine ndikuyangʼanabe ndinaona “mipando yaufumu ikukhazikitsidwa, ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake. Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana; tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje. Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto, ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto. Onani mutuwo |
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.