Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 7:8 - Buku Lopatulika

8 Ndinali kulingilirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga ina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pake zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndinali kulingilirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga ina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pake zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Ndikulingalira za nyangazo, ndinaona nyanga ina, yocheperapo, imene inkatuluka pakati pa zinzake. Zitatu mwa nyanga zoyamba zija zinazulidwa mwa icho. Nyanga iyi inali ndi maso a munthu ndi pakamwa pamene pankayankhula zodzitama.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 7:8
15 Mawu Ofanana  

Yehova adzadula milomo yonse yothyasika, lilime lakudzitamandira;


Ndipo mfumu idzachita monga mwa chifuniro chake, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse nidzanena zodabwitsa pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzachitidwa ukaliwo; pakuti chotsimikizika m'mtimacho chidzachitika.


Pamenepo ndinafuna kudziwa choonadi cha chilombo chachinai chija chidasiyana nazo zonsezi, choopsa chopambana, mano ake achitsulo, ndi makadabo ake amkuwa, chimene chidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ake;


amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.


Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,


Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;


Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.


Ndipo ndinaimirira pa mchenga wa nyanja. Ndipo ndinaona chilombo chilinkutuluka m'nyanja, chakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ndi iwiri, ndi pa nyanga zake nduwira zachifumu khumi, ndi pamitu pake maina a mwano.


Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukachita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolide, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.


Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa