Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,
Mateyu 27:1 - Buku Lopatulika Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa kutacha, akulu onse a ansembe ndi akulu a Ayuda adapanga upo kuti aphe Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmamawa, akulu a ansembe onse ndi akuluakulu anavomerezana kuti aphe Yesu. |
Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,
Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.
Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.
Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.
Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.
Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasakaniza mwazi wao ndi nsembe zao.
Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao,
Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.
Ndipo atamva ichi, analowa mu Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa a bwalo la akulu a milandu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo.
Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mzinda, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha.
Ndipo Saulo anatumiza mithenga kunyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.