Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 18:28 - Buku Lopatulika

28 Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowa ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Adamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita naye ku bwalo la bwanamkubwa. Akuluakulu a Ayuda sadaloŵe nao m'bwalo la bwanamkubwalo, kuwopa kuti angaipitsidwe, pakuti ankafuna kudya phwando la Paska.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Kenaka Ayuda anamutenga Yesu kuchoka kwa Kayafa ndi kupita ku nyumba yaufumu ya bwanamkubwa wa Chiroma. Tsopano kunali mmamawa, ndipo polewa kudetsedwa monga mwa mwambo Ayuda sanalowe mʼnyumba yaufumuyo; iwo anafuna kuti adye Paska.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 18:28
33 Mawu Ofanana  

Pakati pa onyodola pamadyerero, anandikukutira mano.


pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi.


Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.


Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, muzichita Paska, chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri; audye mkate wopanda chotupitsa.


Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.


Pomwepo asilikali a kazembe anamuka naye Yesu kubwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye khamu lao lonse.


Ndipo asilikali anachoka naye nalowa m'bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse.


Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao,


Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.


nayamba kupita naye kwa Anasi; pakuti anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chomwecho.


Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, nalowa pamodzi ndi Yesu, m'bwalo la mkulu wa ansembe;


Chifukwa chake Pilato analowanso mu Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?


Koma muli nao makhalidwe, akuti ndimamasulira inu mmodzi pa Paska; kodi mufuna tsono kuti ndimasulire inu mfumu ya Ayuda?


Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.


Koma linali tsiku lokonza Paska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu!


Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankhe kanthu.


ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa;


Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m'nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m'mbali mwa nyanja.


nanena kuti, Munalowa kwa anthu osadulidwa, ndi kudya nao.


Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;


Ndipo muziphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, ya nkhosa ndi ya ng'ombe, m'malo amene Yehova adzasankha kukhalitsamo dzina lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa