Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 19:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Saulo anatumiza mithenga kunyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Saulo anatumiza mithenga kunyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Usiku womwewo Saulo adatuma anthu kunyumba kwa Davide kuti akambisalire, kuti choncho akamuphe Davide m'maŵa. Koma Mikala, adauza mwamuna wake Davide kuti, “Mukapanda kupulumutsa moyo wanu usiku uno, maŵa muphedwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Usiku womwewo Sauli anatumiza anthu ku nyumba ya Davide kuti akamubisalire ndi kumupha mmamawa. Koma Mikala mkazi wake anamuchenjeza nati, “Ngati usiku uno supulumutsa moyo wako, mawa udzaphedwa.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 19:11
5 Mawu Ofanana  

Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.


Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mzinda, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha.


Ndipo Saulo anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samuele mkulu wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Saulo, ninenera iyonso.


Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa