Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 31:13 - Buku Lopatulika

13 Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Zoonadi, ndimamva anthu ambiri akunong'onezana zoipa za ine, zoopsa zandizinga ponseponse. Amapangana zoti andiwukire, namachita upo woipa woti andiphe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri; zoopsa zandizungulira mbali zonse; iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane, kuti atenge moyo wanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 31:13
21 Mawu Ofanana  

Koma wopereka chikho wamkulu sanakumbukire Yosefe, koma anamuiwala.


Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.


Izizo ziuzungulira pa malinga ake usana ndi usiku; ndipo m'kati mwake muli zopanda pake ndi chovuta.


Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.


Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwe kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye padziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Usatulukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.


Mwaitana zondiopsa mozungulira ngati tsiku la msonkhano; panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova; omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.


Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;


Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;


Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa mu Yudeya yense, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.


Ndipo Saulo anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Yonatani anazindikira kuti atate wake anatsimikiza mtima kupha Davide.


Davide nanena ndi Saulo, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukuchitirani choipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa