Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 1:6 - Buku Lopatulika

ndi Yese anabala Davide mfumuyo. Ndipo Davide anabala Solomoni mwa mkazi wa Uriya;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi Yese anabala Davide mfumuyo. Ndipo Davide anabala Solomoni mwa mkazi wa Uriya;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yese adabereka mfumu Davide. Davide adabereka Solomoni, mwa amene poyamba adaali mkazi wa Uriya.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yese anabereka Mfumu Davide. Ndipo Davide anabereka Solomoni, amene amayi ake anali mkazi wa Uriya.

Onani mutuwo



Mateyu 1:6
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti?


Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa: Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.


Uriya Muhiti; onse pamodzi anali makumi atatu mphambu asanu ndi awiri.


chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti.


Uriya Muhiti, Zabadi mwana wa Alai,


Maina a ana anali nao mu Yerusalemu ndi awa: Samuwa, ndi Sobabu Natani, ndi Solomoni,


Ozemu wachisanu ndi chimodzi, Davide wachisanu ndi chiwiri;


ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.


Ndipo ombadwira mu Yerusalemu ndi awa: Simea, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomoni, anai a Batisuwa mwana wamkazi wa Amiyele;


Mapemphero a Davide mwana wa Yese atha.


Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese, ndi nthambi yotuluka m'mizu yake idzabala zipatso;


ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese;


Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;


ndi Obedi anabala Yese, ndi Yese anabala Davide.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.


Ndipo Saulo anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndili mwana wa kapolo wanu Yese wa ku Betelehemu.


kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe?