Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:58 - Buku Lopatulika

58 Ndipo Saulo anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndili mwana wa kapolo wanu Yese wa ku Betelehemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

58 Ndipo Saulo anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndili mwana wa kapolo wanu Yese wa ku Betelehemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

58 Saulo adafunsa Davide kuti, “Kodi mnyamata iwe, paja ndiwe mwana wa yani?” Davide adayankha kuti, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese, wa ku Betelehemu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

58 Sauli anamufunsa, “Mnyamata iwe, kodi paja ndiwe mwana wayani?” Davide anati, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese wa ku Betelehemu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:58
5 Mawu Ofanana  

Ndipo ananyamula Asahele namuika m'manda a atate wake ali ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi anthu ake anachezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawachera ku Hebroni.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.


Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pachaka ya banja lao lonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa