1 Samueli 22:8 - Buku Lopatulika8 kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Mwina nchifukwa chaketu mukundichita chiwembu chotere. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adandiwululira pamene mwana wanga ankagwirizana ndi mwana wa Yese. Palibe ndi mmodzi yemwe amene akulabadako za ine kapena kundinong'onezako kuti mwana wanga wautsa mtima wa munthu wanga Davide kuti andiwukire, monga akuchitira leromu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Mwinatu nʼchifukwa chake mwagwirizana zondichita chiwembu. Palibe amene anandiwuza pamene mwana wanga ankapanga pangano ndi mwana wa Yese. Palibe aliyense amene ankalabadirako za ine kapena kundiwuza kuti mwana wanga wautsa mtima wa wantchito wanga kuti andiwukire monga wachitira lero.” Onani mutuwo |