Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 22:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake akuima chomzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Yese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yampesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake akuima chomzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Yese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yamphesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndiye Sauloyo adafunsa ankhondo ake aja kuti, “Imvani tsono inu Abenjamini. Kodi mwana wa Yese adzakupatsani minda aliyense mwa inu? Kodi adzakusandutsani atsogoleri a magulu ankhondo nonsenu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Tsono Sauli anafunsa ankhondo ake aja kuti, “Tamverani inu anthu a fuko la Benjamini! Kodi mwana wa Yese adzakupatsani nonsenu minda ndi minda ya mpesa? Kodi nonsenu adzakuyikani kukhala atsogoleri a magulu ankhondo?

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 22:7
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.


Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.


Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvere iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang'aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao.


Ndipo anadza ena a ana a Benjamini ndi Yuda kulinga kwa Davide.


Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese, ndi nthambi yotuluka m'mizu yake idzabala zipatso;


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.


Ndipo Davide anakhala wochenjera m'mayendedwe ake onse; ndipo Yehova anali naye.


Ndipo kunali tsiku lachiwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pake; ndipo Saulo anati kwa Yonatani mwana wake, Mwana wa Yese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?


Pamenepo Saulo anapsa mtima ndi Yonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Yeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?


Ndipo Saulo anati kwa iye, Munapangana chiwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Yese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe?


Pamenepo Doegi wa ku Edomu, anaimirira ndi anyamata a Saulo, nayankha, nati, Ine ndinamuona mwana wa Yeseyo alikufika ku Nobu, kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubi.


Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? Ndi mwana wa Yese ndani? Masiku ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa