Masalimo 99:7 - Buku Lopatulika Iye analankhula nao mu mtambo woti njo: Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye analankhula nao mu mtambo woti njo: Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ankalankhula nawo mu mtambo woima kuti njo. Iwo ankasunga mapangano ndi malangizo amene Iye adaŵapatsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo; iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa. |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
Ndipo kunali, pakulowa Mose m'chihemacho, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa chihemacho; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.
Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la chihema, naitana Aroni ndi Miriyamu; natuluka onse awiri.
Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.
amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.
Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati padziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu.