Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 33:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo kunali, pakulowa Mose m'chihemacho, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa chihemacho; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo kunali, pakulowa Mose m'chihemacho, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa chihemacho; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Mose ataloŵa m'chihema muja, mtambo unkatsika nuphimba pakhomo pa chihemacho, ndipo Chauta ankalankhula ndi Mose kuchokera mumtambomo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Mose akamalowa mu tenti, chipilala cha mtambo chimatsika ndi kukhala pa khomo pamene Yehova amayankhula ndi Mose.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 33:9
17 Mawu Ofanana  

Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kuchokera kwa Abrahamu.


Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.


Iye analankhula nao mu mtambo woti njo: Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.


Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele.


Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.


Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa chihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wake.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.


Ndipo kunali, pakutuluka Mose kunka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chilili, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira atalowa m'chihemacho.


Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu aliyense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikulu zisadye kuphiri kuno.


Ndipo Yehova anatsika mumtambo, naimapo pamodzi ndi iye, nafuula dzina la Yehova.


Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu.


Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, tuluka kunka kuchidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.


Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uli pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha.


Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako.


Ndipo Yehova anaoneka m'chihema, m'mtambo njo; ndipo mtambo njo unaima pa khomo la chihema.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa