Mahema a achifwamba akhala mumtendere, ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima; amene Mulungu amadzazira dzanja lao.
Masalimo 73:3 - Buku Lopatulika Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti ndinkachita nsanje ndi anthu odzikuza, pamene ndidaona anthu oipa akulemera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ndinkachitira nsanje odzitamandira, pamene ndinaona mtendere wa anthu oyipa. |
Mahema a achifwamba akhala mumtendere, ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima; amene Mulungu amadzazira dzanja lao.
Anthu oongoka mtima adzadabwa nacho, ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsutsa wonyoza Mulunguyo.
Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse; maweruzo anu ali pamwamba posaona iye; adani ake onse awanyodola.
Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.
Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.
Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m'chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwake.
Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?
Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.
Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?