Masalimo 70:3 - Buku Lopatulika Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao amene akuti, Hede, hede. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao amene akuti, Hede, hede. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi manyazi poona kuti alephera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,” abwerere chifukwa cha manyazi awo. |
Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.
Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.
nunene kwa ana a Amoni, Tamverani mau a Ambuye Yehova, Atero Ambuye Yehova, Popeza unati, Ha! Kunena malo anga opatulika; muja anadetsedwa ndi kunena dziko la Israele; muja linapasuka ndi kunena nyumba ya Yuda; muja adalowa kundende;
Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Ha! Wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;
Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Ha! Ingakhale misanje yakale ili yathu, cholowa chathu;
(Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphotho ya chosalungama; ndipo anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka;