Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba padziko lapansi ndi pamlengalenga.
Masalimo 69:34 - Buku Lopatulika Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze, nyanja ndi zonse zoyenda m'mwemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze, nyanja ndi zonse zoyenda m'mwemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumwamba ndi pansi pano, nyanja ndi zonse zoyenda m'menemo zitamande Iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye, nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo, |
Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba padziko lapansi ndi pamlengalenga.
Ichi adzachilembera mbadwo ukudza; ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.
Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.
Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.