Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 69:33 - Buku Lopatulika

33 Pakuti Yehova amvera aumphawi, ndipo sapeputsa am'ndende ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Pakuti Yehova amvera aumphawi, ndipo sapeputsa am'ndende ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Paja Chauta amamvera anthu osoŵa, sanyoza anthu ake omangidwa ndi unyolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Yehova amamvera anthu osowa ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 69:33
20 Mawu Ofanana  

Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;


anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lao.


kuti amve kubuula kwa wandende; namasule ana a imfa.


Iwo akukhala mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, omangika ndi kuzunzika ndi chitsulo;


Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.


ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.


Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.


Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.


Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.


Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.


Pakuti atero Yehova kwa nyumba ya Israele, Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo;


Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi moyo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima mu Betele;


Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,


Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu,


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa