Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Masalimo 22:2 - Buku Lopatulika Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza; ndipo usiku, sindikhala chete. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza; ndipo usiku, sindikhala chete. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu wanga, ine ndimalira usana, koma Inu simundiyankha, ndimalira usiku, koma sindipeza mpumulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha, usikunso, ndipo sindikhala chete. |
Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?
Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.
ndi kuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa chikhulupiriro chanu?
Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,