Ndipo dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.
Masalimo 17:4 - Buku Lopatulika Za machitidwe a anthu, ndachenjera ndi mau a milomo yanu ndingalowe njira za woononga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Za machitidwe a anthu, ndachenjera ndi mau a milomo yanu ndingalowe njira za woononga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kunena za ntchito za anthu, ine posunga mau anu, sindidatsate za anthu andeu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kunena za ntchito za anthu, monga mwa mawu a pakamwa panu, Ine ndadzisunga ndekha posatsata njira zachiwawa. |
Ndipo dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.
Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.
Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu, ndi kubisa mphulupulu yanga m'chifuwa mwanga;
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.
Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.
pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?
Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoyamba za zolengedwa zake.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:
Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.
Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.
Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwake, ndi chikho cha madzi, ndipo tiyeni, timuke.
Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa?