Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 4:7 - Buku Lopatulika

7 Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma Yesu adati, “Malembo akutinso, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yesu anamuyankha kuti, “Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 4:7
21 Mawu Ofanana  

Popeza analakalakatu kuchidikhako, nayesa Mulungu m'chipululu.


Ndipo anayesa Mulungu mumtima mwao ndi kupempha chakudya monga mwa kulakalaka kwao.


Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israele.


Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba, osasunga mboni zake;


Pamene makolo anu anandisuntha, anandiyesa, anapenyanso chochita Ine.


Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe. Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?


Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?


Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.


popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;


nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?


Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.


Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la ophunzira goli, limene sanathe kunyamula kapena makolo athu kapena ife?


Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.


Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija.


Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa mu Masa.


chimene makolo anu anandiyesa nacho, ndi kundivomereza, naona ntchito zanga zaka makumi anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa