Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele.
Masalimo 15:4 - Buku Lopatulika M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu, koma amalemekeza anthu omvera Chauta. Ndi amene amachitadi zimene walonjeza, ngakhale zikhale zoŵaŵa chotani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa. Koma amalemekeza amene amaopa Yehova, amene amakwaniritsa zomwe walonjeza ngakhale pamene zikumupweteka, |
Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele.
Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m'chipata cha mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira chotero za iye. Koma Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira.
Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.
Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.
Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako:
Ndipo m'mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.
Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka muimfa kulowa m'moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda akhala muimfa.
Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.