Masalimo 141:3 - Buku Lopatulika Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muike mlonda pakamwa panga, Inu Chauta. Mulonde pa khomo la milomo yanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova ikani mlonda pakamwa panga; londerani khomo la pa milomo yanga. |
Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.
Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala chete osalawa chokoma; ndipo chisoni changa chinabuka.
Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.
Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.