Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:5 - Buku Lopatulika

5 Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Wina asakhulupirire mnansi, asadalire bwenzi lake lapamtima. Aliyense achenjere ndi pakamwa pake, ngakhale polankhula ndi mkazi wake yemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Usadalire mnansi; usakhulupirire bwenzi. Usamale zoyankhula zako ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:5
11 Mawu Ofanana  

Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga.


Inde ndikunga munthu wosamva, ndipo m'kamwa mwanga mulibe makani.


Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.


Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.


Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.


Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Ndipo analira pamaso pake masiku asanu ndi awiriwo pochitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wake mwambiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa