Masalimo 135:8 - Buku Lopatulika Anapanda oyamba a Ejipito, kuyambira munthu kufikira zoweta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anapanda oyamba a Ejipito, kuyambira munthu kufikira zoweta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye amene adapha ana achisamba a ku Ejipito, ana a anthu ndi a nyama omwe, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama. |
Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.
ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.
Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.