Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 127:3 - Buku Lopatulika

Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova, ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

Onani mutuwo



Masalimo 127:3
22 Mawu Ofanana  

Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.


Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.


Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.


Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.


Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakuchulukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao chikhalire.


ndi wachisanu ndi chimodzi Itireamu wa Egila mkazi wa Davide. Awa anambadwira Davide ku Hebroni.


ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.


Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mivi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.


Ndipo anabala ana aamuna asanu ndi awiri, ndi ana aakazi atatu.


Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzachitira chisoni chipatso cha mimba; diso lao silidzaleka ana.


Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.


Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo.


Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.


Ndipo anali nao ana aamuna makumi atatu; ndi ana aakazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ake aamuna ana aakazi makumi atatu ochokera kwina. Ndipo anaweruza Israele zaka zisanu ndi ziwiri.


Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye;