Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Masalimo 118:4 - Buku Lopatulika Anene tsono iwo akuopa Yehova, kuti chifundo chake nchosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anene tsono iwo akuopa Yehova, kuti chifundo chake nchosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu oopa Chauta anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amene amaopa Yehova anene kuti: “Chikondi chake ndi chosatha.” |
Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele.
Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang'ono ndi aakulu.