Masalimo 118:1 - Buku Lopatulika Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha. |
Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.