Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere; nudzazonda za m'banja mwako osasowapo kanthu.
Masalimo 112:3 - Buku Lopatulika M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, ndipo chilungamo chake ndi chosatha. |
Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere; nudzazonda za m'banja mwako osasowapo kanthu.
Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.
Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.
Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.
Ndipo kudzakhala chilimbiko m'nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake.
Pakuti njenjete idzawadya ngati chofunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma chilungamo changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chipulumutso changa kumibadwo yonse.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.