Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga; ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi.
Masalimo 102:9 - Buku Lopatulika Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate, ndi kusakaniza chomwera changa ndi misozi, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate, ndi kusanganiza chomwera changa ndi misozi, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inetu ndimadya phulusa ngati chakudya, chakumwa changa ndimasakaniza ndi misozi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi |
Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga; ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.
Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.
Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wake, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja?
Musachifotokoza mu Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'fumbi.
Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe.